Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 1:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:19
5 Mawu Ofanana  

Kenaka mfumu ya Igupto inayitanitsa azamba aja ndi kuwafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? Bwanji mwasiya ana aamuna kuti akhale ndi moyo?”


Kotero Mulungu anawakomera mtima azambawo, ndipo Aisraeli anapitirirabe kuchulukana nakhala amphamvu kwambiri.


Davide anayankha Ahimeleki kuti, “Mfumu yandituma zinthu zina ndipo yandiwuza kuti, ‘Munthu aliyense asadziwe za zimene ndakutumazo.’ Kunena za anthu anga, ndawawuza kuti tikakumane pamalo pena pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa