Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
Eksodo 1:13 - Buku Lopatulika Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo ankaŵakakamiza mwankhalwe kugwira ntchito yaukapolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anawagwiritsa ntchito mwankhanza kwambiri. |
Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.