Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.
Danieli 8:26 - Buku Lopatulika Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Masomphenya okhudza madzulo ndi mmawa amene unawaona aja ndi woona, koma uwasunge masomphenyawa mwachinsinsi popeza ndi onena za masiku a mʼtsogolo kwambiri.” |
Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali.
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.
Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.
Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.
Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.
Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mau a chinenero cha buku ili; pakuti nthawi yayandikira.