Chivumbulutso 10:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Mabinguwo atangogunda, ndidaati ndilembe. Koma ndidamva mau ochokera Kumwamba akuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi aŵiri aja anena. Usazilembe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.” Onani mutuwo |