Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 7:17 - Buku Lopatulika

Zilombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka padziko lapansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Zilombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi.

Onani mutuwo



Danieli 7:17
9 Mawu Ofanana  

kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:


Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya.


Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.


Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.


Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.