Danieli 3:5 - Buku Lopatulika kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. |
Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yake pansi, nalambira Daniele, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.
Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide;
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?
Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara.