Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.
Danieli 3:16 - Buku Lopatulika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. |
Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.
Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.
Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.
Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.