Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 3:17 - Buku Lopatulika

17 Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 3:17
34 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.


Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi;


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda.


Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.


Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.


Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.


Usaope nkhope zao; chifukwa Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.


Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m'kati mwa moto.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.


Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.


Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.


Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.


Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa