Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 2:49 - Buku Lopatulika

Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.

Onani mutuwo



Danieli 2:49
12 Mawu Ofanana  

Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yachiwiri Mordekai anali wa m'bwalo la mfumu.


Masiku awa pokhala Mordekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.


Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira.


Posekera olungama pali ulemerero wambiri; koma pouka oipa anthu amabisala.


Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.


Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.


Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.


Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi;


Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni.


ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.


Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.