ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.
ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.
Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.
Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,
Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.
Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a mu ufumu wanga sangathe kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.
Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu.