Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
Danieli 2:36 - Buku Lopatulika Ili ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ili ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. |
Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu;
Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fanoli linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsa.