Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.
Danieli 2:29 - Buku Lopatulika Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. |
Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.
Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa,
Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.
Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.
koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa:
Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.
Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi.
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.