Danieli 2:29 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. Onani mutuwoBuku Lopatulika29 Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. Onani mutuwo |
Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa. “Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”