Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya,
Danieli 2:17 - Buku Lopatulika Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. |
Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya,
Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo.
Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.