Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula;
Danieli 12:9 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anandiyankha kuti, “Pita iwe Danieli, pakuti mawuwa ndi osungidwa ndi omatidwa kufikira nthawi ya chimaliziro. |
Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula;
Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.
Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.
Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?
Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.
Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.