Ndi mfumu ya kumwera idzawawidwa mtima, nidzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lake.
Danieli 11:5 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mfumu ya kummwera idzakhala yamphamvu, koma mmodzi mwa akalonga ake adzakhala ndi mphamvu kuposa iyo; adzalamulira ufumu wake waukulu kwambiri. |
Ndi mfumu ya kumwera idzawawidwa mtima, nidzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lake.
Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera, ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.
Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.
Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.
Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera.