ndipo ndidzabweza undende wa Ejipito, ndi kuwabwezera kudziko la Patirosi, kudziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka.
Danieli 11:42 - Buku Lopatulika Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka. |
ndipo ndidzabweza undende wa Ejipito, ndi kuwabwezera kudziko la Patirosi, kudziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka.
Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.
Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake.
Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula.
Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.