Danieli 11:19 - Buku Lopatulika Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zikadzatha izi, mfumu idzabwerera ku malo otetezedwa a dziko la kwawo koma idzapunthwa ndi kugwa osapezekanso. |
Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.
Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.
Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pamtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa.
ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, chinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova.
Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa;