Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzapambana.
Danieli 11:13 - Buku Lopatulika Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza mfumu ya kumpoto idzasonkhanitsa gulu lina lankhondo, lochulukirapo kuposa loyamba; ndipo patapita zaka zingapo idzabwera ndi chigulu chachikulu cha nkhondo chokonzekeratu ndi zida. |
Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzapambana.
Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera, ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.
Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.
Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, ndipo zimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.