Danieli 4:16 - Buku Lopatulika16 Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, ndipo zimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Maganizo ake a umunthu asinthidwe ndipo apatsidwe maganizo a nyama ya kuthengo, mpaka zaka zisanu ndi ziwiri zitadutsa. Onani mutuwo |
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.