chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.
Danieli 1:6 - Buku Lopatulika Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. |
chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.
chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.
Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeke monga Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu.
Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi;
Pamenepo Ariyoki analowa naye Daniele kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja.
Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda?
Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri: