Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 8:8 - Buku Lopatulika

Ndipo ku Beta ndi ku Berotai mizinda ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuchokera ku Beta ndi ku Berotai, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu Davide inatenga mkuwa wambiri kuchokera ku Beta ndi Berotai, mizinda ya Hadadezeri.

Onani mutuwo



2 Samueli 8:8
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.


Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba.


Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.


Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.


Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.


golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe.


napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.


Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere-Hatikoni ndiwo kumalire a Haurani.