Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.
2 Samueli 8:7 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. |
Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.
Ndipo ku Beta ndi ku Berotai mizinda ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.
Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.
Natenga Davide zikopa zagolide zinali pa anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.