Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.
2 Samueli 5:21 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ake nawachotsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ake nawachotsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Afilisti adasiya mafano ao kumeneko, ndipo Davide ndi anthu ake adatenga mafanowo napita nawo kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga. |
Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga.
Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m'menemo ndi mtendere.
Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi.
ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto.
Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.