Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.
2 Samueli 3:26 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu atachokako kwa Davide kuja, adatuma amithenga kuti amlondole Abinere. Iwowo adakampezadi ku chitsime cha Sira, nambweza, Davide osadziŵa kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza amithenga kutsatira Abineri, ndipo anabwera naye kuchokera ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanadziwe zimenezi. |
Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu.
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.