Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.
2 Samueli 3:23 - Buku Lopatulika Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yowabu ndi ankhondo onse amene anali nawo adabwera, ena adauza Yowabuyo kuti, “Abinere mwana wa Nere adaabwera kwa amfumu, ndipo amfumuwo adamlola kuti apite, mwakuti wapitadi mwamtendere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere. |
Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.
Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi.
Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino, ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima.
ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.