Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero.
2 Samueli 3:19 - Buku Lopatulika Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abinere adalankhulanso ndi anthu a fuko la Benjamini. Kenaka adakauzanso Davide ku Hebroni zonse zimene Abenjamini ndi Aisraele adavomerezana kuti achite. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abineri anayankhulanso nawo yekha anthu a fuko la Benjamini. Kenaka anapita ku Hebroni kukamuwuza Davide zonse zimene Aisraeli ndi fuko lonse la Benjamini amafuna kuchita. |
Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero.
Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo.
Ndi a ana a Efuremu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.
Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.