Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.
2 Samueli 24:22 - Buku Lopatulika Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Arauna adauza Davide kuti, “Mbuyanga mfumu, mutenge mukapereke nsembe zinthu zimene zikukomereni. Nazi ng'ombe zokaperekera nsembe yopsereza. Nazinso zipangizo zomangira ng'ombe pamodzi ndi magoli omwe a ng'ombezo, kuti zikhale nkhuni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni. |
Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.
numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho.
Ndipo galetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.