Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:8 - Buku Lopatulika

Koma mfumu inatenga ana aamuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana aamuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho mfumuyo idatenga Arimoni ndi Mefiboseti winanso, ana a Rizipa, mwana wamkazi wa Aya amene adambalira Saulo. Idatenganso ana aamuna asanu amene Merabi, mwana wamkazi wa Saulo, adambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati.

Onani mutuwo



2 Samueli 21:8
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga?


ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako.


Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;


Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake.