Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:5 - Buku Lopatulika

Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwo adayankha kuti, “Saulo adaafuna kutiwonongeratu, ndipo adaakonza zoti titheretu m'dziko lonse la Israele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli,

Onani mutuwo



2 Samueli 21:5
5 Mawu Ofanana  

Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.


Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.