Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
2 Samueli 21:18 - Buku Lopatulika Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake nkhondo idabukanso ndi Afilisti ku Gobu. Pamenepo Sibekai Muhusa, adapha Safu, amene analinso mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai. |
Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.
Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.
Wachisanu ndi chitatu wa mwezi wachisanu ndi chitatu ndiye Sibekai Muhusa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai.