Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.
2 Samueli 20:18 - Buku Lopatulika Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mkazi uja adati, “Paja anthu kale ankati, ‘Kapempheni nzeru ku Abele.’ Nkhani zao ankazitha motero. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. |
Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.
Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?