Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu.
2 Samueli 2:30 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu adabwerako kumene adaakathamangitsa Abinere kuja. Atasonkhanitsa anthu onse pamodzi, kudapezeka kuti padasoŵa ankhondo a Davide okwanira 19, pamodzi ndi Asahele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yowabu anabwerera kuchokera kothamangitsa Abineri ndipo anasonkhanitsa ankhondo ake onse. Kupatula Asaheli, panali ankhondo khumi ndi anayi a Davide amene anasowa. |
Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu.
Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abinere, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi.