Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m'mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.
2 Samueli 2:24 - Buku Lopatulika Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, pa njira ya ku chipululu cha Gibiyoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yowabu ndi Abisai adayamba kuthamangitsa Abinere. Ndipo pamene dzuŵa linkaloŵa, adakafika ku phiri la Ama limene lili cha kuno kwa Giya, pa njira yopita ku chipululu cha Gibiyoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni. |
Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m'mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.
Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda.
Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.