Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;
2 Samueli 19:6 - Buku Lopatulika m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa poti inu mumakonda anthu odana nanu, ndipo mumadana ndi anthu okukondani. Lero ndiye mwatiwonetsa poyera kuti akalonga ndi ankhondo anu mulibe nawo kanthu. Ha, ndikudziŵa kuti Abisalomu adakakhala moyo, tonsefe nkufa, inu mukadakondwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. |
Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;
Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.
Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.