Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordani pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphotho yotere?
Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pang'ono kuti ndiwoloke Yordani pamodzi ndi inu amfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere?
Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere?
Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.
Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.