Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:37 - Buku Lopatulika

37 Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mzinda wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Chonde, ingondilolani ine mtumiki wanu ndibwerere kuti ndikafere kumudzi kwathu, pafupi ndi manda a bambo wanga ndi a mai wanga. Koma suyu mwana wanga Kimuhamu, akhale mtumiki wanu. Iyeyu ndiye aoloke pamodzi ndi inu mbuyanga mfumu. Ndipo mumchitire chilichonse chimene chikukomereni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:37
15 Mawu Ofanana  

koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.


chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.


Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordani pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphotho yotere?


Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu.


Chomwecho mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Kimuhamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israele.


koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.


Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.


ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,


ndipo anachoka, natsotsa mu Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa mu Ejipito,


Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.


Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi.


podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa