Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.
2 Samueli 18:30 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pompo mfumu idati, “Patuka, kaime apo.” Iye adapatuka nakaima potero. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu inati, “Ima apo ndipo udikire.” Kotero iye anapita pa mbali nayima pamenepo. |
Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwe ngati kutani.
Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.