Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.
2 Samueli 18:13 - Buku Lopatulika Ndikadachita chonyenga pa moyo wake, palibe mlandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsutsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikadachita chonyenga pa moyo wake, palibe mlandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsutsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwenzi nditanyoza mau a mfumuwo, pomupha mwana wake, ndipo zikadadziŵika, poti palibe kanthu kobisika pamaso pa mfumu, ndipo inu nomwe simukadanditeteza.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo sindikanayika moyo wanga pa chiswe pakuti palibe chimene chimabisika pamaso pa mfumu komanso inu simukanditeteza.” |
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.