2 Samueli 17:3 - Buku Lopatulika ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha, idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” |
Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.
Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.