Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.
2 Samueli 17:21 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, nanka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankhondo aja atapita, anthuwo adatuluka m'chitsime muja, ndipo adakauza mfumu Davide kuti, “Nyamukani, muwoloke mtsinje mofulumira, popeza kuti Ahitofele walangiza anthu ake zokuthirani nkhondo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu aja atapita, awiriwo anatuluka mʼchitsimemo ndipo anapita kukawuza mfumu Davide nati kwa iye, “Nyamukani, muwoloke mtsinje msangamsanga. Ahitofele wapereka malangizo akutiakuti kutsutsana nanu.” |
Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani.