Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
2 Samueli 16:14 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mfumu ndi anthu onse amene anali naye, adafika ku Yordani ali otopa kwambiri, napumula kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula. |
Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse aamuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye.
Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.
ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'chipululumo.