Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.
2 Samueli 15:22 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana aang'ono onse amene anali naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Davide adauza Itai kuti, “Chabwino, tiye.” Motero Itai Mgiti uja adaoloka mtsinje wa Kidroni, pamodzi ndi anthu ake, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe amene anali naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye. |
Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.
Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.