2 Samueli 14:29 - Buku Lopatulika Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina adatumiza mau kwa Yowabu opempha kuti amtume kwa mfumu. Koma Yowabu sadafike. Abisalomu adatumizanso mau kachiŵiri, koma Yowabu osafika ndithu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abisalomu anatumiza mawu kwa Yowabu, kumutuma kuti apite kwa mfumu, koma Yowabu anakana kubwera. Kotero anatumizanso mawu kachiwiri, koma Yowabu anakananso. |
Koma Vasiti mkazi wamkuluyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wake unatentha m'kati mwake.