Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana aamuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.
2 Samueli 13:34 - Buku Lopatulika Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo nkuti Abisalomu atathaŵa. Tsono mlonda wapalinga poyang'ana, adangoona anthu ambiri akuchokera ku mseu wa Horonaimu, m'mbali mwa phiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa. Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.” |
Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana aamuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.
Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.
Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.