Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe?
2 Samueli 13:27 - Buku Lopatulika Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana aamuna onse a mfumu apite naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Abisalomu adamkakamiza ndithu mpaka Davide adalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse aamuna a mfumu apite nao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye. |
Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe?
Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.