Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera.
2 Samueli 13:17 - Buku Lopatulika Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo Aminoniyo adaitana mnyamata amene ankamtumikira, namuuza kuti, “Mtulutse mkaziyu, achoke pano, ndisamuwonenso, ndipo upiringidze chitseko iyeyo akatuluka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.” |
Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera.
Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.