Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.
2 Samueli 13:15 - Buku Lopatulika Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Aminoni adayamba kudana naye kwabasi Tamarayo, kotero kuti chidani chake ndi Tamara chidakula kwambiri kuposa chikondi chimene adaamkonda nacho. Ndipo Aminoniyo adauza Tamara kuti, “Dzuka, kazipita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!” |
Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.
Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera.
Namdzera a ku Babiloni ku kama wa chikondi, namdetsa ndi chigololo chao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wake unafukidwa nao.