Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mzindawo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mzindawo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa.
2 Samueli 12:29 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Davide adasonkhanitsa ankhondo ake onse, ndipo adapita ku Raba, nakauthira nkhondo mzindawo, nkuulanda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. |
Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mzindawo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mzindawo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa.
Nachotsa korona pamutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pamutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mzindawo zambirimbiri.
Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,