Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni.
2 Samueli 10:9 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele, naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. |
Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni.
Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.
Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.
Ndipo pocheuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; nafuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.